CSAT yati ndikofunika kulondoloza ndalama za Cyclone Freddy

Advertisement

Bungwe la Centre for Social Accountability and Transparency (CSAT) layamikira ganizo loti pakhale komiti yapadera yomwe izithandizira kulondoloza thandizo la ndalama ndi zinthu zothandizira anthu omwe anakhudzidwa ndi namondwe wa freddy.

Izi zikudza pomwe mtsogoleri wa zipani zotsutsa Kondwani Nankhumwa, wakhala akupempha boma mobwerezabwereza kuti likhazikitse komiti yapadera yomwe izilondoloza momwe chuma komanso katundu akugwiritsidwira ntchito kufikira anthu oyenera kulandira thandizo.

Mkulu wa bungwe la CSAT, Willy Kambwandira, anati ntchito ya komitiyi ikhala yosiyana ndi ya dipatimenti yoona za ngozi zogwa mwadzidzi (Dodma) chifukwa komitiyi iziyang’ana kwambiri momwe chuma chagwiritsidwira ntchito komanso kuwonetsetsa kuti chithandizo chafika kwa anthu omwe sadalandirebe thandizo kuchokera ku Dodma

A Kambwandira ayamikiranso Dodma pobwera poyera ndikuwulula ndalama ndi zinthu zomwe alandila komanso momwe azigwiritsira ntchito.

Masiku apitawa pakhala pali malipoti omwe amasonyeza kuti anthu ena akumaba katundu ngati chimanga chomwe chimayenera kuthandizira anthu omwe anakhudzidwa ndi namondwe wa freddy ndipo akukhala mmisasa mmaboma a Blantyre, Mulanje ndi ena.

Follow us on Twitter:

Advertisement