Mbiyang’ambe zogwa nawo zili ku CCAP

Advertisement
Chibuku Malawi

Ngakhale mpingo wa CCAP umaletsa kumwa mowa, kafukufuku wasonyeza kuti akhilisitu ampingo wa CCAP mumzinda wa Lilongwe ndi omwe amamwa mowa kwambiri ngati kulibe mawa.

Kafukufuku wasonyeza kuti zidakwa zochuluka mumzinda wa Lilongwe ndi akhilisitu amene amapemphera mpingo wa Church of Central African Presbyterian (CCAP) pomwe mipesa ili pa nambala ya chisanu (5).

Izi ndi malingana ndi zotsatira za kafukufuku yemwe adachitika ndi akatswiri ochokera ku sukulu zaukachenjede za mdziko muno komaso ena ochokera ku sukulu zaukachenjede za mdziko la Australia.

Zotsatira za kafukufukuyu zasonyeza kuti mpingo wa CCAP ndiumene ukusungira mbiyang’ambe zochuluka zedi kuposa mpingo wina uliose  ndipo pambuyo pake pa kubwera mpingo wa katolika.

Zotsatirazi zomwe akuti kafukufuku wake anachitika mchaka cha 2021 mumzinda wa Lilongwe, zasonyeza kuti mwa anthu zana limodzi (100) omwe amamwa mowa, anthu 31 amakhala akhilisitu a mpingo wa CCAP, pomwe 29 peresenti ndi akhilisitu a chikatoloka.

Mbali inayi zadziwika kuti 10 peresenti ya zidakwa ku Lilongwe, ndi anthu osakhulupirira kuti kuli Mulungu, 9 peresenti ndi mamembala ampingo wa Assemblies of God, pomwe 5 peresenti akuti ndi anthu opemphera mpingo wa Seventh Day Adventist, mipesa.

“Pakati pa magulu 12 achipembedzo omwe atchulidwa pa kafukufuku wa pa intaneti, ambiri mwa omwe amamwa mowa mwauchidakwa mumzindawu anali a CCAP (31%), poyerekeza ndi 29% ya Akatolika, 10% ya osakhulupirira kuti kuli Mulungu, 9% mwa mamembala a Assemblies of God, ndi 5% kuchuluka kwa uchidakwa pakati pa mamembala a SDA,” yatelo mbali ina yazotsatira za  kafukufukuyu.

Chomwe chadabwitsa anthu kwambiri ndi chakuti mipingo monga CCAP, Assemblies of God komaso SDA yomwe imatenga kumwa mowa ngati tchimo, yaposa mpingo wa Katolika omwe ku mwa mowa silimatengedwa ngati tchimo kwenikweni.

Zione Telezia Chinoko ndi amene anatsogolera akatswiri ofufuza zaumoyo padziko lonse ochokera ku St. John of God Hospitaller Service, Kamuzu University of Health Sciences ndi Curtin University School of Population Health ya ku Australia, kuchita kafukufukuyu.

Follow us on Twitter:

Advertisement