DoDMA yakana kuti yagula nyemba ndi kapenta wa K200 miliyoni

Advertisement

Nthambi ya boma yowona za ngozi zogwa mwadzidzi ya DoDMA yakana mwantu wagalu malipoti oti yagwiritsa ntchito ndalama yokwana K200 miliyoni kugulira nsomba za kapenta komaso nyemba zopita kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi yakusefukira kwa madzi.

Lachinayi mphekesera zinali ponseponse kuti nthambi ya DoDMA yagula nyemba komaso nsomba za mtundu wakapenta kuchokera mdziko la Tanzania zomwe akuti ndi za ndalama zokwana K200 miliyoni.

Koma poyankhapo pa mphekeserayi, mmodzi mwa akuluakulu a nthambi ya DoDMA a Charles Kalemba omwe lachisanu atulutsa chikalata chofotokoza za nkhaniyi, ati mphekeserazi ndi bodza la mkunkhuniza.

Mumchikalatachi a Kalemba ati nthambiyi yagwiritsa ntchito K7 miliyoni yokha kugulira ndiwo anthu amene akukhala m’malo oyembezera ndipo ati sakudziwa kuti mphekesera ya ndalama yokwana K200 miliyoni yomwe zikukambidwayi, ikuchokera kuti.

Iwo atsutsaso mphekesera zoti nsomba zomwe agula zachokera mdziko la Tanzania ndipo atiso malipoti oti nthambiyi ya yagula nyemba ndiabodza kaamba koti nthambiyi inaunikira kuti mkwabwino kugula ndiwo zomwe sizingavute kuphika.

“Nthambi ya DoDMA yagula matumba 500 a nsomba zowuma za Kapenta za ndalama yokwana K7 miliyoni (kupatula msonkho wowonjezera) kuchokera ku bungwe logulitsa zakudya ndipo zikalata zothandizira zilipo.

“N’zomvetsa chisoni kuti pakati pa khama logwira ntchito limodzi ndi khama lofikira anthu onse okhudzidwa, anthu ena asankha kuchita sewero pa tsoka lomwe lagwera dziko lino pazifukwa zodziwika bwino kwa iwo eni,” yatelo mbali ina ya chikalata cha DoDMA.

Nthambiyi yalangiza anthu mdziko muno kuti asiye mchitidwe ofalitsa nkhani zabodza ponena kuti mchitidwewu uli ndikuthekera kosokoneza ntchito yofikira anthu amene akhudzidwa ndi namondwe wa Freddy.

DoDMA yatsimikizira a Malawi kuti ndalama zomwe ikulandira pano kuchokera ku boma komaso ma bungwe osiyanasiyana, zigwira ntchito yake yothandizira anthu okhawo omwe akhudzidwa ndi namomdwe wa Freddy.

Pofika lachitatu pa 16 March, anthu 326 amwalira potsatira madzi osefukira omwe akhudza madera ambiri akummwera kwa dziko lino zomwe ndi kaamba ka namondwe wa Freddy yemwe anafika mdziko muno loweruka sabata latha.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.