Boma la a Chakwera lakwiyitsa America pa zakatangale

Advertisement
Malawi President Chakwera

Dziko la United states of America lati ndilokhumudwa kuti boma la Tonse motsogozedwa ndi a Lazarus Chakwera silikuonetsa chidwi chofuna kuthana ndi katangale mdziko muno.

Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe ofesi ya Kazembe wa dziko la America kuno ku Malawi latulutsa lero potsatira ganizo la boma lofuna kuchotsa chiletso cha bwalo la milandu chomwe chabwenzeretsa pa ntchito mkulu wa bungwe la ACB a Martha Chizuma.

Chikalatachi chomwe tsamba lino laona, chati chokhumudwitsa chachikulu nchakuti akuluakulu a boma la Malawi akupanga izi ngakhale kuti dziko la America lakhala likukumana nawo kuwapatsa upangiri pamomwe angathetsere katangale ndi ziphuphu mdziko muno.

Kudzera mumchikalatacho chomwe chaikidwa pa tsamba la fesibuku la ofesi ya kazembe wa dzikolo, America yati imapeleka thandizo ku dziko lino pamgwirizano oti, dziko lino lizionetsetsa kuti thandizolo silikuonongedwa mwa njira iliyose.

“Takhala tikukumana ndi akuluakulu a boma kuti azisonyeza chidwi chawo pankhondo yolimbana ndi katangale osati kumema nkhondo pa anthu omwe akutsogolera ntchito yolimbana ndi katangaleyo, koma zonsezi sizinapindule kanthu.

“Mgwirizano wathu pankhani za thandizo lachitukuko cha dziko lino umagona poti Malawi izionetsetsa kuti chuma cha boma kuphatikizapo ndalama za chitukuko, zikugwiritsidwa ntchito moyenera, poyera komaso mopanda chokaikitsa chili chonse,” yatelo America.

Ofesi yakazembeyo yaonjezera kuti zomwe zakhala zikuchitika pa a Chizuma zikubweretsa chikaiko pa dzikolo ngati dziko la Malawi lingakwanitsedi kuthetsa mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu.

Nkhaniyi ikudza pomwe posachedwapa boma kudzera kwa mlembi wake a Colleen Zamba anaimitsa pa ntchito mkulu wa ACB a Chizuma ndipo malingana ndi chikalata chomwe a Zamba anatulutsa, kuimitsidwaku ndikufuna kupeleka mpata kuti a Chizuma ayankhe kaye milandu pa zomwe anayankhula pafoni ndi munthu wina chaka chatha.

Potsatira nkhaniyi, sabata ino bungwe la anthu oyimilira anzawo pa milandu la Malawi Law Society (MLS), linakatenga chiletso ku bwalo la milandu ponena kuti a Chizuma sakuyenera kuimitsidwa ntchito.

Koma mlangizi wa boma pa nkhani za malamulo a Thabo Chakaka Nyirenda ati boma likufuna lichotse chiletso chomwe bungwe la MLS lakatenga ku khothi ponena kuti a Chizuma akuyenera kuimitsidwabe pa ntchito ndipo izi mzomwe zapangitsa dziko la America kuti linyangale.

Follow us on Twitter:

Advertisement