Yawalakwira Cash Madam… a bwalo ati ali ndi mulandu

Advertisement
Dorothy Shonga

Pamene dziko linatangwa ndi kumangidwa kwa Mayi Chizuma, bwalo ku Lilongwe linatangwa ndi kuzenga milandu Mayi Dorothy Shonga komanso mkulu wakale wa MERA, a Collins Magalasi. Ndipo agwa nayo kale round yoyamba.

Oweluza milandu a Patrick Chirwa apeza kuti a Shonga ndi a Magalasi, kudza anthu ena awiri, ali ndi milandu yoti ayankhe yokhudzana ndi nkhani za katangale ku MERA.

A Shonga ndi ena akuganiziridwa kuti adapangitsa a bungwe la MERA kuwapatsa bizinesi mwa chinyengo. Malinga ndi a mbali ya boma amene akuzenga mulandu, ati a Shonga anagwilitsa ntchito kampani yawo ya Vink kuti abere bungwe la MERA.

Kupatula a Shonga ndi a Magalasi, ena amene akuyimbidwa milandu ndi a Patrick Maulidi ndi a Bright Mbewe amene nawo amagwila ku MERA.

Potengela chigamulo chimene chaperekedwa, anthu anayiwa tsopano ayamba kuzengedwa mulanduwu.

Tipezeni pa Twitter

Advertisement