Osamayankhula ndi boma utaima, gwada…apolisi anapinditsa maondo Mayi Chizuma

Advertisement
Chizuma ACB Director

Kunali nkhanza pamene apolisi anapita kukagwila Mayi Martha Chizuma, Malawi24 yapeza choncho. Kupatula kuwakwenyakwenya, ati apolisi amauza a Chizuma kuti asamayankhule nawo chiyimile.

Pa malipoti amene ayalidwa mu nyumba ya malamulo ndi a Kondwani Nankhumwa, ati apolisi anachita ndi Mayi Chizuma monga akuchita ndi chigandanga choopsa. Mwa zina, ati apolisi analetsa Mayi Chizuma kukatenga Magalasi awo a maso komanso kuvala molongosoka.

“Anamupitila Chizuma ngati mbava,” anatelo a Nankhumwa kuuza nyumba ya malamulo.

Malinga ndi lipotili, ati apolisi m’bandakucha omwe anazinga nyumba ya Mayi Chizuma. Kumeneko anakumana ndi wantchito wa pakhomopo ndipo anamuuza kuti akawauze bwana ake kuti kwabwela alendo.

Mayi Chizuma atauzidwa kuti apolisi abwera kuzawatenga ati anapempha kuti avale molongosoka koma apolisi anakana.

“Iwo analengeza kuti ngati a Chizuma sanyamuka okha, a polisi achita kupita kukawaduda ngati mbala,” anatelo a Nankhumwa kuuza nyumba ya malamulo.

Chipongwe cha a polisi chinakhodzokera pamene a Chizuma anapempha kuti avale magalasi a maso. Apolisi anawakanira.

Ati atafika ku polisi, iwo anawauza kuti agwade ndipo adzipereka bwino sitetimenti yawo ku polisi, ati kuwauza kuti munthu sulankhula ndi boma udakali chiyimire.

“Ngakhale powaitana mayina mammawa omwewu, anawauza kuti agwade, kuwachotsa ulemu,” analira choncho a Nankhumwa.

Tiwoneni pa twitter:

Advertisement