Mukang’amba ticket, kungani ina. Osaonetsa mtima onyanyala – Chakwera

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera wati a Malawi ochuluka akudzinyonga kamba ka mtima wa chifooko.

Polankhula ku Mzuzu pamene anapita kukapemphera, a Chakwera ati a Malawi sakuchedwa kufooka mu nyengo zowawa zomwe akudutsa.

“Anthu ambiri akuzipha chifukwa chotaya chikhulipiliro msanga,” anatero a Chakwera.

Iwo anati anthu aphunzire kulimbikitsana wina ndi mzake kuti asataye chikhulipiliro ndi kufika pozikhweza.

“Mulungu sangataye anthu ake, ndipo sanatitaye a Malawi. Zinthu zavuta inde koma Mulungu ali nafe,” Chakwera watero.

Chichewa chopatsa mphamvu anthu akufooka chimakondedwa ndi anyamata a njuga (kapena kuti bet) amene amauzana maka akagonja pa masewero a njuga. Iwo amauzana kuti ang’ambe ticket ndi kukunga ina.

Advertisement