Mkulu amene analonjeza zokhululukila okuba nkhuku atha kukakhala ku ndende

Advertisement

Ukayenda siya phazi, mulomo umatsata. Mawu awa atha kukhala ndi amene akulingalira a Saulos Chilima pamene atoledwa ndi a polisi poganizilidwa kuti anachita za katangale ndi a Zunneth Sattar.

Bungwe lothetsa ziphuphu la ACB, lamanga wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima kamba kokhudzidwa ndi nkhani za katangale.

Malinga ndi chikalata chimene atulutsa a bungweli, a Chilima akuganiziridwa kuti anachita madilu ndi mkulu wa ma business a Sattar.

A Chilima amene amatsogolera chipani cha UTM chimene chili mu mgwilizano olamula amangidwa ku mmawa kuno atafunsidwa mafunso ochuluka ndi bungwe lothetsa katangale.

Mwa zina, a Chilima akuganizilidwa kuti anapanga ziphuphu zokhudzana ndi ndalama pafupifupi 300 million zokhudzana ndi a Sattar.

Malinga ndi malipoti, bungwe la ACB lalemba ntchito a Mordecai Msiska kuti awathandize kuimba mlandu a Chilima.

Nthawi ya kampeni, a Chilima adauza anthu kuti akazatenga boma azakhululukira akaidi omwe anaba nkhuku ndipo azapititsa ku ndende akaidi oba ndalama zikuluzikulu.

Pakali pano, a bwalo apatsa belo a Chilima.

Advertisement