Tisiyileni Buluma timuthyole khosi – achinyamata a MCP

Advertisement
Malawi Oil Company Buluma

Mdima umene a Malawi ena anauona mu utsogoleri wa chipani cha MCP wayandikanso pamene a chinyamata a chipanichi ati akufuna kupha Helen Buluma.

Malinga ndi mchezo wa pa makina a Intaneti a WhatsApp umene wafala pa bwalo la Fesibukhu, achinyamata ena a mu MCP akuona kuti Mayi Buluma akuyenda atafa kale.

Izi amakambilana Mayi Buluma ataulula kuti akulu akulu a boma akhala akufuna kuchita za katangale kuchoka ku NOCMA.

Mayi Buluma anaulula izi pamene anakumana ndi aphungu ena a nyumba ya malamulo.

“Ntchito yanga ku NOCMA yakhala pa chiopsezo, ndakhala ndikuopsezedwa ndi anthu ena a MCP kuphatikizapo phungu wina a Onani,” anatelo a Buluma.

Mwa zina, iwo anaonjezelapo kuti mlembi wamkulu mu ofesi ya a Chakwera a Colleen Zamba nawo akhala akuwapatsa phuma lokhotetsa zinthu ndi cholinga chofuna kuchita katangale.

Phungu wa chipani chotsutsa cha DPP a Mayi Mary Navitcha anapempha kuti Mayi Buluma apatsidwe chitetezo.

Pothilira ndemanga pa zimenezi mu kachipinda kawo komata pa WhatsApp, achinyamata a Kongeresi anati Mayi Buluma ndi opusa chifukwa sangawapatse chitetezo.

“Ndipo ndingonenelatu kuti zikavuta a Buluma autse mu mtendere,” anatero wachinyamata wina.

Zokambilanazi zadzetsa mantha kwa a Malawi amene akumbukila nkhanza za MCP ya pa dzana imene imapha anthu otsutsana nawo.

Advertisement