Chepetsani kuyendayenda – Kachaje auza a Malawi pamene a Matola ati mafuta sanavute kwenikweni

Advertisement
Kachaje

Mkulu woyang’anila bungwe loona za mphamvu la MERA, a Henry Kachaje auza a Malawi kuti asiye kaye zoyendayenda ndi cholinga chofuna kupulumutsa mafuta a galimoto.

Polankhula pa msonkhano wa atolankhani umene bungwe lawo lachititsa mu boma la Lilongwe, a Kachaje anati kupezeka kwa mafuta kukuyenela kulongosoka pofika lachitatu sabata la mawa.

“Tikunena pano, ma thankala ena ali mnjira ndi mafuta, pofika lachitatu muona kuti zinthu zikusintha,” anatelo a Kachaje. Iwo anaonjezelapo kuti podikila kuti zinthu zilongosoke, a Malawi akuyenela kuchepetsa ma ulendo.

“Ndimangofuna kuwapempha a Malawi kuti pali ma ulendo ena omwe si ofunika kwenikweni, bwanji titawasiya kaye osayenda kuti mafuta atikwanile,” anatelo a Kachaje.

Iwo amayankhula izi ngakhale kuti a Malawi ambiri akhala akudandaula ndi ma ulendo a mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera omwe pakali pano ali mu dziko la Iguputo.

Poyankhula pa msonkhano omwewu, nduna yoona za mphamvu a Ibrahim Matola anati kusowa kwa mafuta kwa lero sikukufanana ndi kwa zaka zammbuyo.

“Mafuta akusowa inde koma bola lero kusiyana ndi mu 2012 mmene anasowanso, anthu anavutika kwambiri,” anatelo a Matola.

A Malawi akhala akugona mu ma filling station kudikila mafuta amene ayamba kusowa. Izi ati zachitika chifukwa cha kusowa kwa ndalama ya kunja.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.