Bola kwa Farao: Afrobarometer yati a Malawi ochuluka atha kuvotela DPP

Advertisement

Ngati mu chipululu nthawi ya Mose, khamu la a Malawi likuti bola ku Aiguputo komkuja. Ulendo wa ku Kenani otsogoleledwa ndi Tonse uja ukuoneka waomba khoma. Tsogolo palibe. Utsogoleri wake ndi opatsa khambi.

Kafukufuku amene bungwe la Afrobarometer anachita mu mwezi wa February, ati anaonetsa kuti a Malawi ochuluka ndi okonzeka kuvotelanso chipani cha DPP. Malinga ndi lipoti la kafukufuku uyu, a Malawi oposa 40 pa handilede alionse anati patachitika masankho iwo voti yawo aponyela chipani cha DPP.

Chipani cha Kongeresi chinali chotsatila, ndipo a Malawi ongopyola pang’ono 25 pa handilede alionse ndiwo anati atha kuvotela Kongeresi. Chipani cha UTM ndiye chaoneka ngati chokutha ngati makatani. Pa anthu handilede alionse anafunsidwa, anthu mwina 8 okha ndiwo anati azafela mbendela ya UTM.

Kafukufuku uyu anaonetsa kuti a Malawi ena adakali mu chigwa cha malingalilo osankha ngati angafunenso kuti ma cadet abwelele kapena Chakwera apitilize. Iwo anati sakudziwa chipani chovotela pomwe ena anakana kutchula kuti angavotele ndani.

A katswiri ena odziwa za kafukufuku ati zotsatila izi zitha kusintha kwambiri makono pamene boma la a Chakwera laphotcholelatu. Mwa zina, iwo atchulapo kugwa kwa ndalama ya Kwacha ndi kusalongosoka kwa magetsi ngati zinthu zina zimene zingagwetse a Chakwera kwa mnanu.

Follow us on Twitter:

Advertisement

One Comment

Comments are closed.