Mphunzitsi wa Flames ndi opanda nzeru, watero Gwamba

Advertisement

Katswiri oyimba nyimbo za chamba cha hip-hop Gwamba wanena kuti mphunzitsi wa timu ya dziko lino Marian Mario Marinica ndiopanda nzeru kamba kosapereka mpata okwanira kwa Peter Banda.

Mukulankhula kwake kudzela pa samba la mchezo la Facebook, Gwamba wanena kuti mphunzitsi oganiza mwanzeru sangalephere kupereka mpata kwa mnyamata waluso ngati Peter Banda.

“Pano tikambe zampira. Coach wa nzeru sangamasiye mwana uyu pa bench,” watero Gwamba

Marinica wakhala asakumugwiritsa ntchito Banda amene amakankha chikopa mu timu ya Simba ya ku Tanzania, ngakhale wakhala akusewera mochotisa kaso.

Mu mpikisano wa Cosafa wa chaka chino, Banda ndi osewera amene wachita bwino kwambiri. Mu masewera omaliza amene Flames idapindirana ndevu mkamwa ndi timu ya dziko la Mauritius la mulungu lapitali, Banda adasankhidwa kukhala osewera amene adachita bwino kuposa onse.

Mnyamata ameneyu amene ali ndi zaka 21, adasewerapo ma timu a Chitawira Rangers ndi Big Bullets, asadapite ku Moldova komwe amkasewera timu ya Sheriff Tiraspol komanso ku Simba.

Follow us on Twitter:

Advertisement

One Comment

  1. Gwamba sakulakwitsa ai zmene akunena ndi zoona ndthu, mkulu amenei ata cha nzeru a kuchita ku mbali ya frames kma misonkho yathu a kungo kudya ali pheee, tisanayambe ma afcon qualifications, munthu amenei ndi nzake Walter asiye pansi maudindo awo if it’s not we’re going to demonstrate,, adalakwanji meck Mwase, chikhale chifukwa kut amakana za chinyengo 😢🚮🚮

Comments are closed.