Zauchifwamba zitha kuchitika ku Malawi, boma la UK lachenjeza

Advertisement

Boma la United Kingdom lachenjeza kuti anthu ena ayesera kuchita zauchifwamba kuno ku Malawi.

Mu uthenga wa pa intaneti, dzikoli lauza nzika zake kuti pali chiopsezo chokuti ziwawa zitha kuchitika ku Malawi.

Langizio la zauchifwambazi ladza potengera zomwe lapeza bungwe lomwe limayang’ana za zauchifwamba ndi uchigawenga ku UK ko.

“Pali chiopsezo  choti nthu ena a zauchifwamba ayesera kuchita ziwawa ku Malawi,” uthengawu watero.

Poyankhulapo, Kazembe wa dziko la Britain ku Malawi a David Beer ati dziko lawo limakhala likuwunika za m’mene chiliri chiopsezo cha zauchifwamba ku Malawi ndipo lapeza kuti panopa chiopsezochi chilipo.

“Izi timapangira chitetezo cha nzika zathu komanso kuti zikamayenda zizikhala ndi uthenga okwanira,” anatero a Beer.

Advertisement