Chaka chino kuli njala, laopseza motero boma

Advertisement

Boma kudzera ku bungwe losunga chakudya la National Food Reserve Agency (NFRA) lati lili ndi chimanga chochepa mu nkhokwe zake, zomwe zikupeleka chiopsezo kuti njala ivuta chaka chino.

Malingana ndi mkulu wa bodi yoyang’anira bungweli a Dennis Kalekeni, nkhokwe za bungweli zimayenera kukhala ndi chimanga chokwana matani 217,000 koma pano kuli matani 30,000 okha.

Iwo anaonjezera kunena kuti chimanga chilipochi chikugwiritsidwa ntchito pothandizira anthu amene akuvutika chifukwa chakusefukira kwa madzi mu madera ambiri mdziko muno.

Kusefukira kwa madziku komwe kwachitika kwambiri mu chigawo cha kum’mwera kwaononga chakudya komanso mbewu zomwe anthu anadzala ndipo pali chiopsezo chakuti anthu ambiri avutika ndi njala.

Malingana ndi lipoti la bungwe lowona za ngozi zogwa mwadzidzi la DODMA, ma banja oposa 200,000 anakhudzidwa ndi kusefukila kwa madzi komwe kunachitika mu February chaka chino.

Advertisement