Khonsolo ya Blantyre yaletsa malonda a Chimanga chachiwisi

Advertisement
Green Maize Malawi

Wolemba: Gracious Zinazi

Khonsolo ya mzinda wa Blantyre yaletsa malonda a chimanga chootcha, chophika ngakhalenso chachiwisi.

Izi ndi malinga ndi chikalata chomwe watulutsa mkulu wa khonsoloyi a Dr Alfred W.D Chanza.

Khonsoloyi yanenetsa kuti onse ochita malonda a chimanga chachiwisi akuyenera kutsatira chiletsochi ndipo ngati satero, azatengeredwa ku bwalo la milandu chifukwa uku ndikuphwanya malamulo oyendetsera mzindawu.

Makhonsolo amakonda kuletsa malonda a chimanga chachiwisi chaka chilichonse ngat njira yochepetsa umbamva wa chimanga mu minda ya anthu.

Advertisement