DPP ipepese pakuphedwa kwa anthu pa zionetselo za 2011 – CCAP Livingstonia

Advertisement

Sinodi ya Livingstonia mu mpingo wa Church of Central Africa Presbyterian (CCAP) yauza chipani chotsutsa boma cha DPP kuti chipepese kumtundu wa a Malawi pakuphedwa kwa anthu pa zionetsero za pa 20 July, 2011.

Izi ndimalingana ndi mlembi wa mkulu ku sinodiyi m’busa William Tembo yemwe amayankhula ku manda a Zolozolo mumzinda wa Mzuzu pamwambo okumbukira anthu omwe anaphedwa pa zionetsero zamchaka 2011.

Anthu mchaka cha 2011 anachita zionetselozi posakondwa ndi ulamuliro wa mtsogoleri wa dziko lino panthawi omwe anali malemu Bingu Wa Mutharika ndipo pazionetselozi anthu 18 anaphedwa pomwe ambiri anavulazidwa.

Ndipo malingana ndi a Tembo, ndikofunika kuti chipani cha DPP chomwe chimalamulira dziko lino panthawiyi, chipepese kumtundu wa a Malawi komaso kumawanja ofedwa pazomwe zina chitikazi.

Iwo anati izi zitha kuthandiza kuchotsa mkwiyo omwe mawanja ofeledwawa amakhala nayo komaso ati ichi chitha kukhala chiyambi chamgwirizano wa bwino pakati pa a Malawi.

“Tsogolo la a Malawi lili kwaife tonse, kaya amene ankalamulira kale, kaya amene akulamulira pano, mipingo, mafumu tonsefe Malawi uno ndiwathu choncho ndikuona ngati ndi kwabwino amene anapangitsa zimeneziwa atabwera poyera ndikupepesa.

“Ife tikadakonda kuti pakachitika zinthu ngati zimenezi pazikhala kukambirana kwa mbali zonse zokhudzidwa kuti mabala obwera kaamba kazinthu zonga izi azipola nsanga komaso kuti tiziyang’ana zopita chitsogolo,” watelo Tembo.

M’mawu ake, yemwe anati mlendo olemekezeka pamwambowu, a Khumbo Kachali omwe anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, anati ndikofunika kuti pakhale mgwirizano wa bwino pakati pa akuluakulu aboma ndi anthu kuti zotelezi zisazachitikeso.

Advertisement