Boma alipempha kutukula ulakatuli

Advertisement
Hudson Chamasowa

M’modzi mwa anthu opanga ndakatulo m’dziko muno a Hudson Chamasowa apempha boma kuti lilowelerepo pa ntchito yolimbikitsa ndikutukula luso la ulakatuli.

Poyankhula ndi nyuzi ino, a Chamasowa anati boma pakali pano likulephera kuvomereza luso la ulakatuli ndipo anati ngati boma litaika chidwi paulakatuli, pali zinthu zambiri zomwe lingapindule.

Mkuluyu anati monga luso loimba, ulakatuli uli ndikuthekela kobweletsa chuma m’dziko muno komaso zitha kuthandizira kupititsa patsogolo chikhalidwe chathu ngati dziko choncho ndikofunika kuti boma liganizilepo bwino pa lusoli.

Iwo anati pakadali pano ulakatuli ukupikisana ndi luso la maimbidwe ndipo boma likuyenera kuganizila zoti alakatuli azilandila kangachepe kuchokera kunyumba zoulitsila mawu monga momwe zimachitikira ndi ayimba.

Apa a Chamasowa anati boma likuyenera kulamulira kuti bungwe loyang’anira oyimba la Copyright Association of Malawi (COSOMA) liyambe kumatoleraso ndalama kuchokera kumawailesi omwe amaulutsa ndakatulo zomwe zizithandiza alakatuliwo eni.

“Dziko la Malawi likulephera kuvomereza luso la ndakatulo ngakhale kuti ili ili ndiluso limodzi lomwe likupikisana ndi maimbidwe. Mutha kuona kuti kukakhala ma show a ndakatulo kumakhala anthu ochuluka kumafanana ndima show a maimbidwe komano a boma sakulitukula lusoli. Boma likulephela kuzindikira kuti ulakatuli ndiofunika kwambiri.

“Tinakakonda boma lizitithandiza ife alakatuli. Kuli bungwe la COSOMA, limene lija likuyenera kumatithandizaso ife monga limachitira ndioyimba. M’mbuyomu amatithandiza ndi a Norwegian Embassy atangosiya iwowo mpaka pano palibe amene amathandizaso gulu la alakatuli choncho tikupempha boma kuti litiganizile ife alakatuli,”anatero Chamasowa.

Mlakatuliyu wapemphaso boma kuti liganizire zoyambitsa maphunziro a ulakatuli loyima palokha m’masukulu kuyambira ku primary, secondary komaso ku university ndicholinga choti lusoli lipite patsogolo.

Apa a Chamasowa anati kuyambitsa phunziloli m’ma sukulu kutha kuthandiza kuti anthu ayambe kuika chidwi chochuluka pa lusoli ndiposo ati izi zitha kuthandiza kuti anthu azitha kuzindikila ndakatulo yeniyeni kapena yabodza.

Advertisement