MEC yakagwada ku khoti la apilu pankhani yazotsatira za chisankho

Advertisement

Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lakamang’ala kubwalo lamilandu lalikulu pachigamulo cha bwalo lamilandu la malamulo pankhani yokhudza zotsatila za chisankho zapitazi.

Mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Lazarus Chakwera komaso mtsogoleri wa United Transformation Movement (UTM) a Saulos Chilima, akufuna kuti bwalori ligamule kuti zotsatila zazisankho zapitazi zinali zosavomerezeka.

Iwo ati izi ndikaamba koti pachisankhochi panachitika mavuto ochuluka choncho a Mutharika sanapambane ngakhale kuti MEC inaulutsa kuti ndi omwe apambana ndipo ati akufuna kuti pachitike chisankho china.

Koma mulanduwu ulimkati kumvedwa, mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika anakasuma kupempha kuti bwalo lamilanduli lithetse mulanduwu ponena kuti a Chakwera ndi a Chilima anatengera mulanduwu Ku bwalori nthawi yomwe amapatsidwa itatha.

Popeleka chigamulo ngati nkoyemera kuthetsa mulanduwu lachisanu sabata yatha, bwalo lamilandu pankhani za malamuloli linagamula kuti mulanduwu omwe a Mutharika amafuna uthetsedwe, upitilire kumvedwa Ku bwalo lamilanduli.

Koma potsutsana ndichigamulochi bungwe la MEC kudzera mwa oliyimilira pa milandu, Lolemba lakagwada kubwalo lamilandu lalikulu mdziko muno kuti ligamule kuti chigamulo cha bwalo lamalamulori ndicholakwika.

Bungweli lati chigamulo chomwe bwalo la milandu la malamulo linapeleka chili ndi zolakwika zambiri ndipo akufuna kuti chigamulochi chichotsedwe ndipo mulanduwu uthetsedwe monga momwe akufunila mtsogoleri wa dziko linoyu.

Pakadali pano mtsogoleri wa chipani cha MCP komaso aphungu ake akunyanyala zokambilana zanyumba ya malamulo pomwe akupitilira kutsutsa kuti a Mutharika ndi omwe anapambana pazisankho zapa May 21 zi.

Advertisement