Iphani owotcha makala – Winiko

Advertisement
Charcoal Malawi

Mmutu mwa phungu wa Kum’mwera kwa boma la Mulanje a Bon Kalindo otchuka kuti Winiko muli chilango chimodzi basi pa mlandu ulionse, kupha basi.

Patapita nthawi a Kalindo atapempha boma kuti lizipha anthu onse okupha anthu a khungu la chi albino, pano a Kalindo aona anthu ena oyenela kuphedwa. Amenewa ndi owotcha makala.

Bon Kalindo
Bon Kalindo: Apheni basi mukawapeza.

Malinga ndi a Kalindo, anthu onse opezeka akuotcha makala akuyenela kuphedwa, chandamale ya pompo pompo.

“Anthu amenewa akuononga dziko lino, angodula mitengo ndi kumabweletsa mavuto osiyanasiyana. Apheni basi mukawapeza,” anatelo a Kalindo.

Iwo ananena izi mu nyumba ya malamulo ku mayambililo a sabata lino.

Koma a bungwe la Forum for National Development adzudzula kolimba a Kalindo. Iwo ati a Kalindo aziyankhula ngati m’dindo. “A Kalindo ndi phungu, akuyenela kudziwa kuti anthu ngakhale olakwila malamulo ali ndi ufulu,” anatelo a Flyson Chodzi a bungweli.

Advertisement

One Comment

  1. winiko winiko winiko, yankhula ngati munthu wamkulu iwe. Kodi kuotcha makala ndi tchimo losakhululukidwa????????????????????????? iwe kwanu umaphikira makala umawatenga kuti. Ndimayesa umagula kwa anthu omwewa?????????????????? musamayakhule motumbwa mwava. ili ndi dziko mukakwela mwamba musanyoze omwe ali pansi. Ukafuna uziphe wekha chifukwa cha uhule wako uja wonyenga ndi ana omwe. Akulu inu chigololo chepesani

Comments are closed.