Macelba wasintha mayankhulidwe pa Malawi ndi Apse Mtima

Advertisement

Katswiri oyimba chamba cha hip hop Macelba watenga gawo lalikulu kuti malankhulidwe a Chichewa asinthe m’dziko lino ndi nyimbo yake ya Apse Mtima.

Nyimboyi yomwe yatuluka chaka chomwe chino yagwedeza dziko la Malawi. Ana, amayi ndi abambo agwa m’chikondi ndi mayimbidwe amenewa zomwe zapangisa kuti malankhulidwe awo asinthe.

Macelba, m’mene amkajambula Kanema wa apse mtima.

Panopa a Malawi akumakonda kugwiritsa ntchito mawu oti “Apse Mtima” akamacheza kapena kulemba pa makina a intaneti.

zikumakhala chonchi anthu akamanena za chinthu chinachake chomwe akufuna azichita, monga m’mene Macelba akunenera mu nyimboyi.

Walusoyu mu gawo limodzi la nyimbo yake akunena kuti kumapemphera, satana azipsa mtima. Potengera ndi m’mene anthu aganizira, akumaphatikiza mawu osiyasiyana ndi mawu oti Apse Mtima.

Anthu othilira ndemanga pa nkhani zosiyanasiyana anena kuti izi zikubweretsa poyera mphamvu zomwe akatswiri a za msangalutso alinazo.

Monga katswiri wina oyimba, Vube, anasinthaso malankhulidwe ndi nyimbo yake ya Chindekha. Awa ndi mawu amene akumagwiritsidwa ntchito kwambiri masiku ano.

Macelba amene dzina lake lenileni lili Smart Banda, akunka nasangalatsa a Malawi ndi nyimboyi kudzeranso pa kanema. Apse mtima inajambulidwa mu mzinda wa Lilongwe.

Banda ndi m’modzi wa oyimba amene amakondedwa kwambiri ndi a Malawi. Nyimbo zake zambiri a Malawi anagwa nazo m’chikondi.

Ena omukonda akuti, “mverani nyimbo za Macelba kuti nyimbo zosasangalasa zipse mtima”

Advertisement